2 Chronicles 18:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udati, ‘Ndidzapita, nkumakanena zabodza kudzera mwa aneneri ake onse.’ Pamenepo Chauta adati, ‘Ukakatero, ukakhozadi. Pita ukamnyengerere.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nuti uwu, Ndidzatuluka ndi kukhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati Iye, Udzamnyengadi, nudzakhoza; tuluka, ukatero kumene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzimuwo unati, “Ine ndidzapita ndi kukhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse!” Yehova anati, “ ‘Iwe ukamunyengadi iyeyo. Pita kachite zimenezo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nuti uwu, Ndidzaturuka ndi kukhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ace onse. Nati Iye, Udzamnyengadi, nudzakhoza; turuka, ukatero kumene.