2 Chronicles 18:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Zedeki uja, mwana wa Kenana, adadza pafupi namenya Mikaya pa tsaya, namufunsa kuti, “Kodi mzimu wa Chauta udadzera njira iti kuti uchoke mwa ine, uzikalankhula ndi iwe?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anayandikira, nampanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji kulankhula ndi iwe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi ndi kumenya khofi Mikaya. Zedekiya anafunsa kuti, “Kodi mzimu wochokera kwa Yehova unadzera njira iti pamene unachoka kwa ine kupita kwa iwe?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anayandikira, nampanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandicokera bwanji kulankhula ndi iwe?