2 Chronicles 18:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Ine ndidzizimbayitsa, ndipo ndipita kunkhondoko, koma iwe uvale malaya ako aufumu.” Choncho mfumu ya ku Israele idadzizimbayitsa, onsewo nkupita ku nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu valani zovala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israele, namuka iwo kunkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya Israeli inati kwa Yehosafati, “Ine ndipita ku nkhondo modzibisa koma iwe uvale mikanjo yaufumu.” Kotero mfumu ya Israeli inadzibisa ndipo inapita ku nkhondoko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu bvalani zobvala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israyeli, namuka iwo kunkhondo.