2 Chronicles 18:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Siriya nkuti italamula oyendetsa magaleta kuti asamenye nkhondo ndi wina aliyense, wamng'ono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israele basi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu ya Aramu tsono idauza akapitao a magaleta ake, ndi kuti, Musayambana ndi ang'ono kapena akulu, koma ndi mfumu ya Israele yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mfumu ya Aramu inalamulira olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu koma mfumu ya Israeli yokha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu ya Aramu tsono idauza akapitao a magareta ace, ndi kuti, Musayambana ndi ang'ono kapena akuru, koma ndi mfumu ya Israyeli yekha.