2 Chronicles 18:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene oyendetsa magaletawo adaona Yehosafati, adati, “Ndithudi ameneyo ndiye mfumu ya ku Israele.” Choncho adabwerera kudzalimbana naye. Koma Yehosafati adayamba kufuula, ndipo Chauta adamthandiza. Mulungu adaŵabweza m'mbuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Olamulira magaleta ataona Yehosafati, iwo anaganiza kuti, “Mfumu ya Israeli ndi iyi.” Kotero anatembenuka kukamenyana naye koma Yehosafati anafuwula, ndipo Yehova anamuthandiza. Mulungu anawabweza mʼmbuyo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pamene akapitao a magareta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israyeli. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anapfuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapambukitsa amleke.