2 Chronicles 18:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu wina adakoka uta wake mwachiponyeponye, ndipo adalasa mfumu ya ku Israele pa maluma a malaya ake achitsulo. Pamenepo mfumuyo idauza woyendetsa galeta lake kuti, “Bwerera, undichotse pankhondo pano chifukwa ndavulazidwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu anaponya muvi wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israeleyo pakati pa maluma a malaya ake achitsulo. Potero anati kwa woyendetsa galetayo, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kukhamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndipo analasa mfumu ya Israeli pakati polumikizira malaya achitsulo. Mfumu inawuza oyendetsa galeta kuti, “Bwerera, undichotse pa nkhondo pano. Ndavulazidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu anaponya mubvi wace ciponyeponye, namlasa pakati pa maluma a maraya ace acitsulo. Potero anati kwa woyendetsa garetayo, Tembenuza dzanja lako, nundicotse ku khamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.