2 Chronicles 18:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhondo idakula kwambiri tsiku limenelo, mwakuti mfumu ya ku Israeleyo idangokhala tsonga m'galeta lake itayang'anana ndi Asiriya mpaka madzulo. Motero pamene dzuŵa linkaloŵa, idafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nkhondo inakula tsiku lija; koma mfumu ya Israele inagwirizizika m'galeta wake popenyana ndi Aaramu mpaka madzulo, namwalira nthawi yakulowa dzuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nkhondo inakula kwambiri tsiku lonse, ndipo mfumu ya Israeli inakhala tsonga mʼgaleta lake kuyangʼanana ndi Aaramu mpaka madzulo. Ndipo pamene dzuwa linkalowa inamwalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nkhondo inakula tsiku lija; koma mfumu ya Israyeli inagwirizizil ka m'gareta wace popenyana ndi Aaramu mpaka madzulo, namwalira nthawi yakulowa dzuwa.