2 Chronicles 18:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu ya ku Israele idasonkhanitsa aneneri ake 400, ndipo idaŵafunsa kuti, “Kodi ife tipite kukamenyana nkhondo ndi Ramoti-Giliyadi, kaya kapena ineyo ndileke?” Aneneriwo adamuuza kuti, “Pitani, pakuti Mulungu aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mfumu ya Israeli inasonkhanitsa aneneri 400 ndipo inawafunsa kuti, “Kodi tipite kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?” Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Mulungu adzawupereka mʼdzanja la mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu ya Israyeli anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Gileadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.