2 Chronicles 18:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Alipo wina amene angapemphe nzeru kwa Chauta, dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imila. Koma ine ndimadana naye ameneyo popeza kuti sandilosera zabwino, nthaŵi zonse amangondilosera zoipa.” Tsono Yehosafati adati, “Iyai mfumu, musatero.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Imila. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife kudzera mwa iye titha kufunsira kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa sandilosera zabwino koma zoyipa nthawi zonse. Iyeyu ndi Mikaya mwana wa Imula.” Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu isanene motero.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Yimla. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.