2 Chronicles 18:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu ya ku Israele idaitana imodzi mwa nduna nkuiwuza kuti, “Takaitanani Mikaya, mwana wa Imila, abwere kuno msanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu ya Israele inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Imila.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa akuluakulu ake ndipo inati, “Kamutengeni Mikaya mwana wa Imula, abwere msanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu ya Israyeli inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Yimla.