2 Chronicles 18:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu ya Israele tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zachifumu zao, nakhala pamalo popondera mphesa pakhomo pa chipata cha Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, atavala mikanjo yawo yaufumu anali atakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopunthira tirigu pa khomo la chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu ya Israyeli tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wacifumu wace, obvala zobvala zacifumu zao, nakhala pamalo poyera polowera pa cipata ca Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.