2 Chronicles 19:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakakhala mlandu wokhudza abale anu amene akukhala m'mizinda yao, monga mlandu wokhetsa magazi, kapena mlandu wa kusamvera malamulo kapena malangizo kapena zogamula zina, muziŵaphunzitsa nthaŵi zonse kuti asamachimwe pamaso pa Chauta. Motero mkwiyo wa Chauta sudzakugwerani inuyo ndi abale anu. Muzichita choncho, ndipo simudzachimwa konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ukakudzerani mlandu uliwonse wochokera kwa abale anu okhala m'midzi mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa chilamulo ndi chiuzo, malemba ndi maweruzo, muwachenjeze kuti asapalamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzapalamula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ukakudzerani mlandu uli wonse wocokera kwa abale anu okhala m'midzi mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa cilamulo ndi ciuzo, malemba ndi maweruzo, muwacenjeze kuti asaparamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzaparamula.