2 Chronicles 19:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Amariya, mkulu wa ansembe, ndiye adzakhale wokutsogolerani pa zonse zokhudza Chauta. Zebadiya mwana wa Ismaele, kazembe wa fuko la Yuda, ndiye aziyang'anira zonse zokhudza mfumu. Ndipo Alevi adzakutumikirani ngati akapitao. Muzichita zimenezi molimba mtima, Chauta akhale naye amene ali wolungama.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, Amariya wansembe wamkulu, ndiye mkulu wanu m'milandu yonse ya Yehova; ndi Zebadiya mwana wa Ismaele, wolamulira nyumba ya Yuda, m'milandu yonse ya mfumu; ndi Alevi akhale akapitao pamaso panu. Chitani molimbika mtima, ndipo Yehova akhale ndi abwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Amariya, mkulu wa ansembe adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza Yehova, ndipo Zebadiya mwana wa Ismaeli, mtsogoleri wa fuko la Yuda, adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza mfumu ndipo Alevi adzatumikira ngati okuyangʼanirani. Muchite molimba mtima ndipo Yehova akhale ndi iwo amene adzachita bwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, Amariya wansembe wamkuru, ndiye mkuru wanu m'mirandu yonse ya Yehova; ndi Zebadiya mwana wa Ismayeli, wolamulira nyumba ya Yuda, m'mirandu yonse ya mfumu; ndi Alevi akhale akapitao pamaso panu. Citani molimbika mtima, ndipo Yehova akhale ndi abwino.