2 Chronicles 19:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mneneri Yehu, mwana wa Hanani, adatuluka kuti akumane naye, ndipo adafunsa mfumu Yehosafati kuti, “Kodi ndi bwino kuŵathandiza anthu oipa amene amadana ndi Chauta? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Chauta ulikudza kwa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mlosi Yehu, mwana wa Hanani, anatuluka kukakumana naye ndipo anati kwa mfumu, “Kodi nʼkoyenera kuthandiza oyipa ndi kukonda iwo amene amadana ndi Yehova? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Yehova uli pa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naturuka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza oipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Cifukwa ca ici ukugwerani mkwiyo wocokera kwa Yehova.