2 Chronicles 19:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku Yerusalemuko Yehosafati adaika Alevi ena ndi ansembe ndiponso akulu a mabanja a Aisraele, kuti aziweruza m'dzina la Chauta ndi kugamula milandu ya anthu. Iwoŵa ankakhala ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehosafati anaikanso m'Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akulu a nyumba za makolo m'Israele, aweruzire Yehova, nanena milandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu Yerusalemu, Yehosafati anasankha Alevi ena, ansembe ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli kuti aziyangʼanira Malamulo a Yehova ndi kuweruza milandu. Ndipo iwo amakhala mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehosafati anaikanso m'Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akuru a nyumba za makolo m'Israyeli, aweruzire Yehova, nanene mirandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu.