2 Chronicles 2:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adayankha Solomoni pomulembera kalata yonena kuti, “Chifukwa chakuti Chauta amakonda anthu ake, wakuika iweyo kuti ukhale mfumu yao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anayankha ndi kulembera, natumiza kalatayo kwa Solomoni, ndi kuti, Powakonda anthu ake Yehova anakulongani mfumu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hiramu, mfumu ya ku Turo, anamuyankha Solomoni pomulembera kalata kuti, “Chifukwa Yehova amakonda anthu ake, wayika iwe kukhala mfumu yawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Huramu mfumu ya Turo anayankha ndi kulembera, natumiza kalatayo kwa Solomo, ndi kuti, Powakonda anthu ace Yehova anakulongani mfumu yao.