2 Chronicles 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatinso, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, amene adapatsa mfumu Davide mwana wanzeru, waluntha, ndi womvetsa zinthu bwino, woti amange nyumba ya Chauta ndiponso nyumba yaufumu ya iye mwini wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Hiramu anawonjezera kunena kuti, “Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi! Iye wamupatsa Davide mwana wanzeru, wodzaza ndi luntha ndi wozindikira, amene adzamanga Nyumba ya Mulungu ndi kudzimangira yekha nyumba yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wace.