2 Chronicles 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
amene mai wake ndi wa ku Dani, ndipo bambo wake anali wa ku Tiro. Iyeyo ndi wodziŵa bwino ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, miyala, ndi matabwa, ndiponso nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso bafuta wosalala. Angathe kuchitanso ntchito zonse zozokota, ndi ntchito ina iliyonse imene mungampatse kuti achite pamodzi ndi anthu anu aluso, anthu aluso a mbuyanga Davide bambo wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana akazi a Dani, ndipo atate wake ndiye munthu wa ku Tiro, wodziwa kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira chopanga chilichonse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
amene amayi ake anali wochokera ku Dani ndipo abambo ake anali a ku Turo. Iye anaphunzitsidwa kugwira ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, miyala yokongola ndi matabwa, ndiponso nsalu zofewa zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Alinso ndi luso la zosemasema ndipo atha kupanga chilichonse chimene wapatsidwa. Iye adzagwira ntchito ndi amisiri anu ndi a mbuye wanga, Davide abambo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana akazi a Dani, ndipo atate wace ndiye munthu wa ku Turo, wodziwa kucita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira copanga ciri conse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu.