2 Chronicles 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ife tidzadula mtengo uliwonse wa ku Lebanoni umene mungaufune, ndipo tidzakutumizirani mitengoyo poimanga pamodzi ndi kuiyandamitsa pa nyanja mpaka ku Yopa, kuti inuyo muitenge ndi kupita nayo ku Yerusalemu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ife tidzadula mitengo yonse imene mukuyifuna kuchokera ku Lebanoni ndipo tidzayimanga pamodzi ndi kuyiyadamitsa pa madzi mpaka ku Yopa. Ndipo inu mudzatha kuyitenga mpaka ku Yerusalemu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebano monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.