2 Chronicles 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Solomoni adaŵerenga alendo onse amene anali m'dziko lonse la Israele, monga momwe bambo wake Davide adaaŵaŵerengera kale. Ndipo padapezeka anthu okwanira 153,600.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anawerenga alendo onse okhala m'dziko la Israele, monga mwa mawerengedwe aja atate wake Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anawerenga alendo onse amene anali mu Israeli, potsatira chiwerengero chimene abambo ake Davide anachita ndipo panapezeka kuti analipo anthu 153,600.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anawerenga alendo Onse okhala m'dziko la Israyeli, monga mwa mawerengedwe aja atate wace Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.