2 Chronicles 2:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapatula anthu 70,000 kuti akhale amtengatenga, ndipo anthu 80,000 kuti akhale okumba miyala ku mapiri. Tsono anthu 3,600 adaŵaika kuti akhale akapitao ogwiritsa anthu ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika zikwi makumi asanu ndi awiri za iwowa asenze mirimo, ndi zikwi makumi asanu ndi atatu ateme m'mapiri, ndi akapitao zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi agwiritse anthu ntchito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayika anthu 70,000 kuti akhale onyamula katundu ndi anthu 80,000 kuti akhale ophwanya miyala mʼmapiri, anthu 3,600 anawayika kukhala akapitawo oyangʼanira anthu pa ntchitoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika zikwi makumi asanu ndi awiri za iwowa asenze mirimo, ndi zikwi makumi asanu ndi atatu ateme m'mapiri, ndi akapitao zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndilimodzi agwiritse anthu nchito.