2 Chronicles 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatumiza mau kwa Hiramu mfumu ya ku Tiro, adati, “Monga momwe munkachitira ndi Davide bambo wanga, pomamtumizira mitengo ya mkungudza, kuti amangire nyumba yake yoti azikhalamo, muchitenso momwemo ndi ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anatumiza kwa Huramu mfumu ya Tiro, ndi kuti, Monga momwe munachitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundichitire ine momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anatumiza uthenga uwu kwa Hiramu mfumu ya ku Turo: “Munditumizire mitengo ya mkungudza monga munachitira ndi abambo anga pamene munawatumizira mitengo ya mkungudza yomangira nyumba yaufumu yokhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anatumiza kwa Huramu mfumu ya Turo, ndi kuti, Monga momwe munacitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundicitire ine momwemo.