2 Chronicles 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndani angathe kummangira nyumba, poti ku mlengalenga ngakhale kumwambamwamba sikungathe kumkwanira Iye? Kodi ine ndinenso yani kuti ndingammangire nyumba, osati kamalo chabe koti nkumafukizapo lubani pamaso pa Mulungu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndani angathe kumumangira Iye Nyumba, pakuti mlengalenga, ngakhale kumwamba kwenikweni sikungamukwane? Tsono ine ndine yani kuti ndimangire Iyeyo Nyumba, kupatula malo chabe opserezerapo nsembe pamaso pake?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira cofukiza ndiko?