2 Chronicles 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso wodziŵa kuzokota. Akhale pamodzi ndi anthu aluso amene ali ndi ine ku Yuda ndi ku Yerusalemu amene Davide bambo wanga adandipatsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine m'Yuda ndi m'Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, nsalu yapepo ndi yofiira ndi yobiriwira ndiponso waluso losema, kuti adzagwire ntchito mu Yuda ndi Yerusalemu pamodzi ndi anthu aluso amene abambo anga Davide anandipatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono munditumizire munthu wa luso lakucita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota ziri zonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine m'Yuda ndi m'Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.