2 Chronicles 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munditumizirenso mitengo ya mkungudza, mitengo ya mlombwa ndiponso matabwa ambaŵa a ku Lebanoni, poti ndikudziŵa kuti anyamata anu amadziŵa kudula mitengo ku Lebanoni. Ndipo anyamata anga adzakhala pamodzi ndi anyamata anu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munditumizirenso mitengo yamikungudza, ndi yamlombwa, ndi yambawa, ya ku Lebanoni; pakuti ndidziwa kuti anyamata anu adziwa kutema mitengo m'Lebanoni; ndipo taonani, anyamata anga adzakhala ndi anyamata anu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Munditumizirenso mitengo ya mkungudza, payini ndiponso matabwa a mʼbawa wa ku Lebanoni, pakuti ndikudziwa kuti anthu anu ali ndi luso locheka matabwa kumeneko. Antchito anga adzagwira ntchito pamodzi ndi antchito anu
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munditumizirenso mitengo yamikungudza, ndi yamlombwa, ndi yambawa, ya ku Lebano; pakuti ndidziwa kuti anyamata anu adziwa kutema mitengo m'Lebano; ndipo taonani, anyamata anga adzakhala ndi anyamata anu,