2 Chronicles 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuti andidulire mitengo yochuluka, popeza kuti nyumba imene ndimangeyo idzakhala yaikulu ndi yochititsa kaso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiko kundikonzera mitengo yambirimbiri; pakuti nyumbayi nditi ndiimange idzakhala yaikulu ndi yodabwitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti andipatse matabwa ambiri, chifukwa Nyumba imene ndikumanga iyenera kukhala yayikulu ndi yokongola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiko kundikonzera mitengo yambirimbiri; pakuti nyumbayi nditi ndiimange idzakhala yaikuru ndi yodabwitsa.