2 Chronicles 20:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu pamene Aisraele ankachoka ku Ejipito, simudalole kuti aŵathire nkhondo Aamoni, Amowabu ndi anthu a ku phiri la Seiri. Onsewo adaŵaleka osaŵaononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalola Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma tsopano pano pali anthu ochokera ku Amoni, Mowabu ndi Phiri la Seiri amene dziko lawo Inu simunawalole Aisraeli kuti alithire nkhondo pamene amabwera kuchokera ku Igupto. Kotero anatembenuka ndi kuwaleka ndipo sanawawononge.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Moabu, ndi a ku phiri la Seiri, amene simunalola Israyeli awalowere, pakuturuka iwo m'dziko la Aigupto, koma anawapambukira osawaononga;