2 Chronicles 20:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m'Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Tamverani mfumu Yehosafati ndi onse amene amakhala mu Yuda ndi Yerusalemu! Zimene Yehova akunena kwa inu ndi izi: ‘Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha gulu lalikulu lankhondo ili. Pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m'Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa cifukwa ca aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.