2 Chronicles 20:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sikudzafunika kuti mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale m'malo mwanu, mungoima, ndipo muwonerere Chauta akukumenyerani nkhondo, inu anthu a ku Yuda ndi inu anthu a mu Yerusalemu.’ Musaope ndipo musataye mtima, mutuluke maŵa mukalimbane nawo, Chauta adzakhala nanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Si kwanu kuchita nkhondo kuno ai; chilimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Si kwanu kucita nkhondo kuno ai; cirimikani, imani, nimupenye cipulumutso ca Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwaturukire, popeza Yehova ali ndi inu.