2 Chronicles 20:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yehosafati adazyolikitsa nkhope yake pansi, ndipo anthu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yerusalemu adagwa pansi pamaso pa Chauta nampembedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala m'Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehosafati anaweramitsa nkhope yake ndi kugunda pansi, ndiponso anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anagwa pansi ndi kulambira Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehosafati anawerama mutu wace, nkhope yace pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala m'Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.