2 Chronicles 20:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena adadzauza Yehosafati kuti “Chinamtindi cha anthu chikudzamenyana nanu nkhondo, kuchokera ku Edomu patsidya pa nyanja. Anthuwo ali ku Hazazoni-Tamara,” (ndiye kuti Engedi).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ena anabwera kudzamuwuza Yehosafati kuti, “Gulu lalikulu kwambiri lankhondo likubwera kudzachita nanu nkhondo lochokera ku Edomu, ku mbali ina ya Nyanja. Gululi lafika kale ku Hazazoni Tamara” (ndiye kuti Eni-Gedi).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukuru wa anthu ocokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni Tamara, ndiwo Engedi.