2 Chronicles 20:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ataŵafunsa anthuwo, adasankha ena oti aziimbira Chauta ndi kumtamanda, oimbawo atavala zovala zoyera, akutsogolera gulu lankhondo namanena kuti, “Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafunsira kwa anthu, Yehosafati anasankha anthu oti ayimbire Yehova ndi kumutamanda chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake pamene amapita ali patsogolo pa gulu la ankhondo, akunena kuti: “Yamikani Yehova pakuti chikondi chake ndi chosatha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oyimbira Yehova, ndi kulemekeza ciyero cokometsetsa, pakuturuka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti cifundo cace cikhala cosatha.