2 Chronicles 20:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo aja atayamba kuimba ndi kutamanda, Chauta adaŵatchera msampha Aamoni, Amowabu ndiponso anthu a ku phiri la Seiri, amene adaadzalimbana ndi anthu a ku Yuda, kotero kuti adaŵagonjetsa onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo poyamba iwo kuyimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amoabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.