2 Chronicles 20:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aamoni ndi Amowabu adaukira anthu okhala ku phiri la Seiri, naŵaononga kotheratu. Ndipo ataononga anthu onse a ku Seiri aja, adayamba kumaphana okhaokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ana a Amoni, ndi a Mowabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala m'Seiri, anasandulikirana kuonongana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu anawukira anthu ochokera ku Phiri la Seiri, ndipo anawawononga ndi kuwatheratu. Atatsiriza kuwapha anthu ochokera ku Seiri anamenyana wina ndi mnzake mpaka kuwonongana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ana a Amoni, ndi a Moabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala m'Seiri, anasandulikirana kuonongana.