2 Chronicles 20:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake anthu a ku Yuda atafika ku nsanja yakuchipululu, adapenya kumene kunali chinamtindi cha anthu chija. Adangoona mitembo yokhayokha ili pansi ngundangunda. Panalibe ndi mmodzi yemwe wopulumuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kuchipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo ili ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Yuda atafika pa malo oyangʼanana ndi chipululu ndi kuona kumene kunali gulu lalikulu lankhondo, iwo anangoona mitembo yokhayokha itagona pansi ndipo palibe amene anathawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kucipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo iri ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.