2 Chronicles 20:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehosafati ndi anthu ake atadzafunkha za anthuwo, adapeza ng'ombe zambirimbiri, katundu, zovala ndiponso zinthu zamtengowapatali. Adatenga zinthu zochuluka, mpaka kuzilephera. Adafunkha zinthuzo masiku atatu, chifukwa zinali zambirimbiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha, ndipo pakati pawo anapeza katundu wambiri ndi zovala ndiponso zinthu zina zamtengowapatali kuposa zomwe akanatha kunyamula. Kunali katundu wambiri kotero kuti zinawatengera masiku atatu kuti amutenge.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ace kutenga zofunkha zao, anapezako cuma cambiri, ndi mitembo yambiri, ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinacuruka.