2 Chronicles 20:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zonse zimene adachita Yehosafati kuyambira poyamba mpaka potsiriza, zidalembedwa m'buku la mbiri ya Yehu, mwana wa Hanani, limene lili chigawo cha buku lokamba za mafumu a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m'buku la mafumu a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zochitika zina zokhudza ufumu wa Yehosafati, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la Yehu mwana wa Hanani, zomwe zikupezeka mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Macitidwe ena tsono adazicita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wochulidwa m'buku la mafumu a Israyeli.