2 Chronicles 20:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Eliyezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa, adalosa zoipira Yehosafati adati, “Chifukwa chakuti mwagwirizana ndi Ahaziya, Chauta adzaononga zimene mwapangazo.” Ndipo zombozo zidaonongekadi zosakafika ku Tarisisi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Eliyezere mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula ntchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliezara mwana wa Dodavahu wa ku Maresa ananenera motsutsana ndi Yehosafati ndipo anati, “Chifukwa chakuti wachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova adzawononga zimene mwapangazo!” Sitima za pamadzizo zinawonongeka ndipo sizinapite nʼkomwe kumene zimakachita malonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Eliezeri mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula nchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisi.