2 Chronicles 20:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adati, “Chauta, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu Wakumwamba? Kodi suja mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu? M'manja mwanu muli mphamvu ndi nyonga, kotero kuti palibe ndi mmodzi yemwe woti nkulimbana nanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? Ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulimbana ndi Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anati: “Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulaka Inu.