2 Chronicles 20:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Choipa chikatigwera mwachilango, monga nkhondo, mlili kapena njala, tidzaima m'Nyumba ino ndiponso pamaso panu, popeza kuti dzina lanu lili m'Nyumba muno. Tsono tidzalira kwa Inu pa mavuto athu, Inuyo mudzamva, ndipo mudzatipulumutsa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chikatigwera choipa, lupanga, chiweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala chilili pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kufuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cikatigwera coipa, lupanga, ciweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala ciriri pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kupfuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.