2 Chronicles 21:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kubzolera pamenepo adayambitsa akachisi opembedzerako mafano ku dziko lamapiri la ku Yuda, ndipo adatsogolera anthu a ku Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, nasokeza anthu a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala m'Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anamanganso malo opembedzerapo mafano mʼmapiri a Yuda ndipo anachititsa anthu a mu Yerusalemu kukhala osakhulupirika. Choncho anasocheretsa anthu a ku Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nacititsa okhala m'Yerusalemu cigololo, nakankhirako Ayuda.