2 Chronicles 21:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma watsata chitsanzo cha mafumu aku Israele. Watsogolera anthu a ku Yuda pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu pochimwitsa anthu a ku Israele. Wapha abale ako a pa banja la atate ako, amene anali abwino kupambana iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma wayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo watsogolera anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kukhala osakhulupirika, monga linachitira banja la Ahabu. Waphanso abale ako, abale a banja la abambo ako, anthu amene anali abwino kuposa iweyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, ndi kucititsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu cigololo, monga umo anacitira cigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;