2 Chronicles 21:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero iwowo adadzalimbana ndi anthu a ku Yuda naŵathira nkhondo. Ndipo adalanda zinthu zonse zimene adazipeza ku nyumba ya mfumu, pamodzinso ndi ana ake aamuna ndi akazi ake, kotero kuti panalibe mwana ndi mmodzi yemwe wamwamuna amene adatsala, kupatula Ahaziya mzime wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda chuma chonse chinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ake omwe, ndi akazi ake, osamsiyira mwana, koma Yehowahazi yekha mwana wake wamng'ono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anathira nkhondo Yuda. Analowanso ndi kutenga katundu yense amene anamupeza mʼnyumba ya mfumu pamodzi ndi ana ake ndi akazi ake. Palibe mwana amene anatsala kupatula mwana wake wamngʼono kwambiri, Ahaziya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda cuma conse cinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ace omwe, ndi akazi ace, osamsiyira mwana, koma Yehoahazi yekha mwana wace wamng'ono.