2 Chronicles 21:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita nthaŵi ndithu, pomatha chaka chachiŵiri, matumbo ake adayamba kusololoka chifukwa cha nthendayo, ndipo adafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu sadasonkhe moto kuti amchitire ulemu monga m'mene ankachitira ndi makolo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, itapita nthawi, pakutha pake pa zaka ziwiri, anatuluka matumbo ake mwa nthenda yake namwalira nazo nthenda zoipa. Ndipo anthu ake sanampserezere zonunkhira, monga umo anapserezera makolo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita nthawi, kumapeto kwa chaka chachiwiri, matumbo ake anatuluka chifukwa cha nthendayo, ndipo anafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu ake sanasonkhe moto kumuchitira ulemu, monga anachitira ndi makolo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, itapita nthawi, pakutha pace pa zaka ziwiri, anaturuka matumbo ace mwa nthenda yace namwalira nazo nthenda zoipa, Ndipo anthu ace sanampserezera zonunkhira, monga umo anapserezera makolo ace.