2 Chronicles 21:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo anali wa zaka 32 pamene ankayamba ufumu wake, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu. Adafa popanda munthu womumvera chisoni. Adamuika mu mzinda wa Davide, koma osati m'manda a mafumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu. Iyeyo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo anamwalira popanda odandawula, nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati mʼmanda a mafumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai.