2 Chronicles 21:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atate ao adaaŵapatsa mphatso zambiri za siliva, golide, ndi zinthu zamtengowapatali, pamodzi ndi mizinda yamalinga ya ku Yuda. Koma ufumu adapatsa Yehoramu, chifukwa chakuti anali mwana wachisamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikulu, zasiliva, ndi zagolide, ndi za mtengo wake, pamodzi ndi midzi yamalinga m'Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wake woyamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abambo awo anawapatsa mphatso zambiri za siliva, golide ndi zinthu zina zamtengowapatali komanso mizinda yotetezedwa ya Yuda. Koma iye anapereka ufumu kwa Yehoramu chifukwa anali mwana wake woyamba kubadwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikuru, za siliva, ndi za golidi, ndi za mtengo wace, pamodzi ndi midzi yamalinga m'Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wace woyamba.