2 Chronicles 21:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankatsata makhalidwe a mafumu a ku Israele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zilizonse pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, pakuti anakwatira mwana wa Ahabu. Ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, umo anacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wace; ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova.