2 Chronicles 22:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu okhala mu Yerusalemu adalonga ufumu Ahaziya, mzime wa Yehoramu uja, m'malo mwa bambo wakeyo, pakuti gulu lankhondo limene lidadza pamodzi ndi Arabu kuzithandoko, linali litapha ana onse akuluakulu aamuna. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda, ndiye amene adaloŵa ufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo okhala m'Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wake wamng'ono akhale mfumu m'malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a mu Yerusalemu anayika Ahaziya mwana wamngʼono kwambiri wa Yehoramu kukhala mfumu mʼmalo mwake, popeza gulu lankhondo limene linabwera ndi Aarabu ku misasa, linapha ana onse aakulu. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo okhala m'Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wace wamng'ono akhale mfumu m'malo mwace; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kucigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda.