2 Chronicles 22:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ataliya, mai wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a pa banja laufumu la Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Ataliya mai wake wa Ahaziya anaona kuti mwana wake adafa, anauka, naononga mbeu yonse yachifumu ya nyumba ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ataliya, amayi ake a Ahaziya, ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakapha onse a banja laufumu la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Ataliya anaona kuti mwana wace adafa, anauka, naononga mbeu yonse yacifumu ya nyumba ya Yuda.