2 Chronicles 22:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu, adatenga Yowasi mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wake wa wansembe Yehoyada, poti anali mlongo wake wa Ahaziya, adambisa mwanayo, kotero kuti Ataliya sadamuphe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehosabati mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wake m'chipinda chogonamo. Momwemo Yehosabati mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wake wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, momuba ndi kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene amati aphedwe ndipo anamuyika iye ndi mlezi wake mʼchipinda chogona. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa wansembe Yehoyada, yemwe anali mlongo wake wa Ahaziya anamubisa mwanayo kuti Ataliya asamuphe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wace m'cipinda cogonamo. Momwemo Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wace wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.